9 Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni.
10 Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
11 Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.
12 Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?
13 Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mudzi wakuti wakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, Ddi kupindula nao;
14 inu amene simudziwa cimene cidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
15 Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzacita kakuti kakuti.