Malaki 1 BL92

Kusayamika kwa Israyeli pa cikondi ca Mulungu

1 KATUNDU wa mau a Yehova wa kwa Israyeli mwa Malaki.

2 Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wace wa Yakobo kodi? ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;

3 koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ace abwinja, ndi kupereka colowa cace kwa ankhandwe a m'cipululu.

4 Cinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawacha, Dziko la coipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao cikwiyire.

5 Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkuru kupitirira malire a Israyeli.

6 Mwana alemekeza atate wace, ndi mnyamata mbuye wace; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?

7 Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

8 Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe coipa! ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe coipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? kapena adzakubvomerezani kodi? ati Yehova wa makamu.

9 Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti aticitire cifundo; icico cicokera kwa inu; kodi Iye adzabvomereza ena a inu? ati Yehova wa makamu.

10 Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto cabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira capereka m'dzanja lanu.

11 Pakuti kuyambira koturukira dzuwa kufikira kolowera kwace dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa cofukiza ndi copereka coona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

12 Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zace, cakudya cace, conyozeka.

13 Mukutinso, Taonani, ncolemetsa ici! ndipo mwacipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu? ati Yehova.

14 Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lace, nawinda, naphera Yehova nsembe cinthu cacirema; pakuti Ine ndine mfumu yaikuru, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.

Mitu

1 2 3 4