1 Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akucita coipa, adzakhala ngati ciputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
2 Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la cilungamo lidzakuturukirani, muli kuciritsa m'mapiko mwace; ndipo mudzaturuka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng'ombe onenepa,
3 Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wamakamu.
4 Kumbukilani cilamulo ca Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliraco m'Horebu cikhale ca Israyeli lonse, ndico malemba ndi maweruzo.
5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikuru ndi loopsa la Yehova.
6 Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.