Malaki 2 BL92

Mau akutsutsa ansembe

1 Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.

2 Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale cifukwa simuliika mumtima.

3 Taonani, ndidzaipsa mbeu cifukwa ca inu, ndi kuwaza ciphwidza pankhope panu, ndico ciphwidza ca nsembe zanu, ndipo adzakucotsani pamodzi naco.

4 Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti cipangano canga cikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.

5 Cipangano canga cinali naye ca moyo ndi ca mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa cifukwa ca dzina langa.

6 Cilamulo ca zoona cinali m'kamwa mwace, ndi cosalungama sicinapezeka m'milomo mwace; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu,

7 Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga cidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna cilamulo pakamwa pace; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.

8 Koma inu mwapambuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'cilamulo; mwaipsa cipangano ca Levi, ati Yehova wa makamu.

9 Cifukwa cace Inenso ndakuikani onyozeka ndi ocepseka kwa anthu onse, popeza simunasunga njira zanga, koma munaweruza mwankhope pocita cilamulo.

Za kukwatira akazi acilendo, Za kuleka mkazi kosayenera

10 Kodi sitiri naye Atate mmodzi ife tonse? sanatilenga kodi Mulungu mmodzi? Ticita monyengezana yense ndi mnzace cifukwa ninji, ndi kuipsa cipangano ca makolo athu?

11 Yuda wacha monyenga, ndi m'Israyeli ndi m'Yerusalemu mwacitika conyansa; pakuti Yuda waipsa cipatuliko ca Yehova cimene acikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mlungu wacilendo.

12 Yehova adzalikha munthu wakucita ici, wogalamutsa ndi wobvomereza m'tnahema a Yakobo, ndi iye wopereka copereka kwa Yehova wa makamu.

13 Ndi ici mubwereza kucicita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso copereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.

14 Koma mukuti, Cifukwa ninji? Cifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamcitira cosakhulupirika, cinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.

15 Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamcitire monyenga mkazi wa ubwana wace ndi mmodziyense.

16 Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi iye wakukuta cobvala cace ndi ciwawa, ati Yehova wa makamu; cifukwa cace sungani mzimu wanu kuti musacite mosakhulupirika.

17 Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi ciani? Ndi ici cakuti munena, Yense wakucita coipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa ciweruzo?

Mitu

1 2 3 4