Malaki 3 BL92

Za mthenga wokonzeratu njira ya Ambuye

1 Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kacisi wace modzidzimutsa; ndiye mthenga wa cipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.

2 Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwace? ndipo adzaima ndani pooneka Iye? pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;

3 ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'cilungamo.

4 Pamenepo copereka ca Yuda ndi Yerusalemu cidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija ndi ngati zaka zoyamba zija.

5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi acigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa nchito pa kulipira kwace, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

6 Pakuti Ine Yehova sindisinthika, cifukwa cace inu ana a Yakobo simunathedwa.

Za kusalanda za Mulungu ndi madalitso atsatapo

7 Kuyambira masiku a makolo anu mwapambuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?

8 Kodi munthu adzalanda za Mulungu? ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzi limodzi la magawo khumi, ndi zopereka.

9 Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.

10 Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

11 Ndipo ndidzadzudzula zolusa cifukwa ca inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zace, zosaca m'munda, ati Yehova wa makamu.

12 Ndipo amitundu onse adzacha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.

13 Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi ciani?

14 Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa cabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wace, ndi kuyenda obvala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?

15 Ndipo tsopano tiwacha odzikuza odala, inde iwo ocita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.

16 Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzace; ndipo Yehova anawachera khutu namva, ndi buku la cikumbutso linalembedwa pamaso pace, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukila dzina lace.

17 Ndipo adzakhala anga anga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wace womtumikira.

18 Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.

Mitu

1 2 3 4