5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi acigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa nchito pa kulipira kwace, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.
6 Pakuti Ine Yehova sindisinthika, cifukwa cace inu ana a Yakobo simunathedwa.
7 Kuyambira masiku a makolo anu mwapambuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?
8 Kodi munthu adzalanda za Mulungu? ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzi limodzi la magawo khumi, ndi zopereka.
9 Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.
10 Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.
11 Ndipo ndidzadzudzula zolusa cifukwa ca inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zace, zosaca m'munda, ati Yehova wa makamu.