13 Anatumiza moto wocokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa;Wachera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo;Wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.
14 Gori la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lace;Zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvuyanga;Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.
15 Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga;Waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga,Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Ziyoni, monga mopondera mphesa.
16 Cifukwa ca zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi:Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditarikira;Ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.
17 Ziyoni atambasula manja ace, palibe wakumtonthoza;Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ace;Yerusalemu wasanduka cinthu conyansa pakati pao.
18 Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwace:Mudtvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone cisoni canga;Anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.
19 Ndinaitanaakundikondawokoma anandinyenga;Ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mudzimu,Alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.