2 Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazicitira cisoni;Wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wace;Wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ace.
3 Pokwiya moopsya walikha nyanga zonse za Israyeli;Wabweza m'mbuyo dzanja lace lamanja pamaso pa adaniwo,Natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.
4 Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo;Wapha onse okondweretsa maso;Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
5 Yehova wasanduka mdani, wameza Israyeli;Wameza zinyumba zace zonse, wapasula malinga ace;Nacurukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi cibumo.
6 Wacotsa mwamphamvu dindiro lace ngati la m'munda;Waononga mosonkhanira mwace;Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi sabata m'Ziyoni;Wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.
7 Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira;Wapereka m'manja a adani ace makoma a zinyumba zace;Iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.
8 Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni;Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo;Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.