9 Zipata zace zalowa pansi; waononga ndi kutyola mipiringidzo yace;Mfumu yace ndi akalonga ace ali pakati pa amitundu akusowa cilamulo;Inde, aneneri ace samalandira masomphenya kwa Yehova.
10 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m'cuuno mwao:Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.
11 Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.
12 Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
13 Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu?Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?
14 Aneneri ako anakuonera masomphenya acabe ndi opusa;Osaulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,Koma anakuonera manenero acabe ndi opambutsa.
15 Onse opita panjira akuombera manja:Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,Kodi uwu ndi mudzi wochedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?