1 Tsoka iwo akulingirira cinyengo, ndi kukonza coipa pakama pao! kutaca m'mawa acicita, popeza cikhozeka m'manja mwao.
2 Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazicotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yace, inde munthu ndi colowa cace.
3 Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndilingirira coipa pa banja ili, cimene simudzacotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; Pakuti nyengo iyi ndi yoipa.
4 Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! andicotsera ili! agawira opikisana minda yathu.
5 Cifukwa cace udzasowa woponya cingwe camaere m'msonkhano wa Yehova.
6 Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzacoka.