1 Kalanga ine! pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.
2 Watha wacifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wace ndi ukonde.
3 Manja ao onse awiri agwira coipa kucicita ndi cangu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza cifukwa ca mphotho; ndi wamkuruyo angonena cosakaza moyo wace; ndipo aciluka pamodzi.
4 Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.
5 Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.
6 Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amace, mpongozi aukira mpongozi wace; adani ace a munthu ndiwo a m'nyumba yace.
7 Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa cipulumutso canga; Mulungu wanga adzandimvera.