4 Koma Yehova anautsa cimphepo cacikuru panyanja, ndipo panali namondwe wamkuru panyanja, ndi combo cikadasweka.
5 Pamenepo amarinyero anacita mantha, napfuulira yense kwa mlungu wace, naponya m'nyanja akatundu anali m'combo kucipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa combo, nagona tulo tofa nato.
6 Ndipo mwini combo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukila tingatayike.
7 Ndipo anati yense kwa mnzace, Tiyeni ticite maere, kuti tidziwe coipa ici catigwera cifukwa ca yani. M'mwemo anacita maere, ndipo maere anagwera Yona.
8 Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu coipa ici catigwera cifukwa ca yani? nchito yako njotani? ufuma kuti? dziko lako nliti? nanga mtundu wako?
9 Ndipo ananena nao, Ndine Mhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba amene analenga nyanja ndi mtunda.
10 Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ici nciani wacicita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.