5 Ndipo anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira cosala, nabvala ciguduli, kuyambira wamkuru kufikira wamng'ono wa iwowa.
6 Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Nineve, ndipo Inanyamuka ku mpando wace wacifumu, nibvula copfunda cace, nipfunda ciguduli, nikhala m'mapulusa.
7 Ndipo analalikira, nanena m'Nineve mwa lamulo la mfumu ndi nduna zace, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;
8 koma zipfundidwe ndi ciguduli munthu ndi nyama, nizipfuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yace yoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwace.
9 Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wace waukali, kuti tisatayike,
10 Ndipo Mulungu anaona nchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka coipa adanenaci kuti adzawacitira, osacicita.