17 Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka colowa canu acitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulunguwao?
18 Pamenepo Yehova anacitira dziko lace nsanje, nacitira anthu ace cifundo.
19 Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ace, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale citonzo mwa amitundu;
20 koma ndidzakucotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira ku dziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwace ku nyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwace ku nyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwace kudzakwera, ndi pfungo lace loipa lidzakwera; pakuti inacita zazikuru.
21 Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wacita zazikuru.
22 Musamaopa, nyama za kuthengo inu; pakuti m'cipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.
23 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula yamyundo, monga mwa cilungamo cace; nakubvumbitsirani mvula, mvula yamyundo ndi yamasika mwezi woyamba.