2 Sanamvera mau, sanalola kulangizidwa; sanakhulupirira Yehova, sanayandikira kwa Mulungu wace.
3 Akalonga ace m'kati mwace ndiwo mikango yobangula; oweruza ace ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.
4 Aneneri ace ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza cilamulo.
5 Yehova pakati pace ali wolungama; sadzacita cosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera ciweruzo cace poyera, cosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.
6 Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungondya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.
7 Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pace pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, nabvunditsa macitidwe ao onse.
8 Cifukwa cace, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.