3 ndi kukumbukila kosalekeza nchito yanu ya cikhulupiriro, ndi cikondi cocitacita, ndi cipiriro ca ciyembekezo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;
4 podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, cisankhidwe canu,
5 kuti Vthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kucuruka kwakukuru; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu cifukwa ca inu.
6 Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'cisautso cambiri, ndi cimwemwe ca Mzimu Woyera;
7 kotero kuti munayamba kukhala inu citsanzo kwa onse akukhulupira m'Makedoniya ndi m'Akaya.
8 Pakuti kuturuka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Makedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse cikhulupiriro canu ca kwa Mulungu cidaturuka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.
9 Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembeoukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weni weni wamoyo,