17 Pakuti, kumva zowawa cifukwa ca kucita zabwino, ndi kumva zowawa cifukwa ca kucita zoipa, nkwabwino kumva zowawa cifukwa ca kucita zabwino, ngati citero cifuniro ca Mulungu,
18 Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu;
19 m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende,
20 imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka cingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;
21 cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu;
22 amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.