3 Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kucita cifuno ca amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
4 m'menemo ayesa ncacilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa citayiko, nakucitirani mwano;
5 amenewo adzamwerengera iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.
6 Pakuti cifukwa ca ici walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m'thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.
7 Koma citsiriziro ca zinthu zonse ciri pafupi; cifukwa cace khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;
8 koposa zonse mukhale naco cikondano ceni ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwiriritsa unyinji wa macimo;
9 mucerezane wina ndi mnzace, osadandaula: