1 PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu monga mwa cilamuliro ca Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi ca Kristu Yesu, ciyembekezo cathu:
2 kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'cikhulupiriro: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Kristu Yesu Ambuye wathu.
3 Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,
4 kapena asasamale nkhani zacabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'cikhulupiriro;
5 koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;
6 zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;