1 Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi ciphunzitso zisacitidwe mwano.
2 Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupira ndi okondedwa, oyanjana nao pa cokomaco, Izi uphunzitse, nucenjeze.
3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosabvomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi ciphunzitsoco ciri monga mwa cipembedzo:
4 iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayarukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zieokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;
5 makani opanda pace a anthu oipsika nzeru ndi ocotseka coonadi, akuyesa kuti cipembedzo cipindulitsa.
6 Koma cipembedzo pamodzi ndi kudekha cipindulitsa kwakukuru;
7 pakuti sitinatenga kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pocoka pano;