3 cimene tidaciona, ndipo tidacimva, tikulatikirani inunso, kuti inunso mukayaniane pamodzi ndi ife; ndipo ciyanjano cathu cirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wace Yesu Kristu;
4 ndipo izi tilemba ife, kuti cimwemwe cathu cikwaniridwe.
5 Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima.
6 Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo siticita coonadi;
7 koma ngati tiyenda m'kuunika, mongalye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzace, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo wonse.
8 Tikati kuti tiribe ucimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe coonadi.
9 Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.