10 Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu.
11 Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo
12 Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife;
13 m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace.
14 Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.
15 Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
16 Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.