12 Mwa ici sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'coonadi ciri ndi inu.
13 Ndipo ndiciyesa cokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;
14 podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Kristu anandilangiza.
15 Koma ndidzacitanso cangu kosalekeza kuti nditacoka ine, mudzakhoza kukumbukila izi,
16 Pakuti sitinatsata miyambi yacabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m'maso ukulu wace.
17 Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;
18 ndipo mau awa ocokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi iye m'phiri lopatulika lija,