9 Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;
10 kama makamaka iwo akutsata zathupi, m'cilakolako ca zodetsa, napeputsa cilamuliro; osaopa kanthu, otsata cifuniro ca iwo eni, santhunthumira kucitira mwano akulu;
11 popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakucita mwano.
12 Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akucitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,
13 ocitidwa zoipa kulipira kwa cosalungama; anthu akuyesera cowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zirema, akudyerera m'madyerero acikondi ao, pamene akudya nanu;
14 okhala nao maso odzala ndi cigololo, osakhoza kuleka ucimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
15 posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya cosalungama;