9 Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.
10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi cibumo cacikuru, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kurentha kwakukuru, ndipo dziko ndi nchito ziri momwemo zidzarenthedwa.
11 Popezaizi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'cipembedzo,
12 akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwace kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha mota idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukuru.
13 Koma monga mwa lonjezano lace tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi ziko latsopano m'menemo mukhalitsa cilungamo.
14 Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.
15 Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu cipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa cwa iye, anakulemberani;