2 lalikira mau; cita nao pa nthawi yace, popanda nthawi yace; tsutsa, dzudzula, cenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi ciphunzitso.
3 Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:
4 ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe.
5 Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, cita nchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.
6 Pakuti ndirimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.
7 Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga cikhulupiriro:
8 cotsalira wandiikira ine korona wa cilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ace.