1 PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Kristu Yesu:
2 Cisomo kwa inu, ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.
3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;
4 monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,