15 Mwa ici inenso, m'mene ndamva za cikhulupiriro'ca mwa Ambuye Yesu ciri mwa inu, cimenenso mufikitsira oyera mtima onse,
16 sindileka kuyamikacifukwa ca inu, ndi kukumbukila inu m'mapemphero anga;
17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire iye;
18 ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero wacolowa cace mwa oyera mtima,
19 ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba,
20 imene anacititsa mwa Kristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, 1 namkhazikitsa pa dzanja lace lamanja m'zakumwamba,
21 2 pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lochedwa, si m'nyengo yinoya pansi pano yokha, komanso mwaiyo ikudza;