15 atacotsa udani m'thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kucitapo mtendere;
16 ndi kuti akayanianitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;
17 ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;
18 kuti mwa iye ife tonse awiri tiri nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.
19 Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;
20 omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa pangondya;
21 1 mwa iye cimango conse, columikizika pamodzi bwino, cikula, cikhale 2 kacisi wopatulika mwa Ambuye;