1 Cifukwa ca ici ine Paulo, ndine wandende wa Kristu Yesu cifukwa ca inu amitundu,
2 ngatitu munamva za udindo wa cisomo ca Mulungucimene anandipatsa ine ca kwa inu;
3 ndi umo anandizindikiritsa cinsinsico mwa bvumbulutso, monga ndinalemba kale mwacidule,
4 cimene mukhoza kuzindikira naco, pakuciwerenga, cidziwitso canga m'cinsinsi ca Kristu,
5 cimene sanacizindikiritsa ana a anthu m'mibadwo yina, monga anacibvumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ace oyera mwa Mzimu,
6 kuti amitundu ali olowanyumbapamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi oland ira nafe pamodzi palonjezano mwa Kristu Yesu, mwa Uthenga Wabino,
7 umene anandikhalitsa mtumiki wace monga mwa mphatso ya cisomo ca Mulungu, cimene anandipatsa ine, monga mwa, macitidwe a mphamvu yace.