1 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
2 ndi kuonetsera kudzicepetsa konse, ndi cifatso, ndi kuonetsera cipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzace, mwa cikondi;
3 ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa cimangiriro ca mtendere.
4 Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi ca maitanidwe anu;