23 koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,
24 2 nimubvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca coonadi.
25 Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace.
26 5 Kwiyani, koma musacimwe; dzuwa lisalowe muli cikwiyire,
27 ndiponso 6 musampatse malo mdierekezi.
28 Wakubayo asabenso; koma 7 makamaka agwiritse nchito, nagwire nchito yokoma ndi manja ace, kuti akhale naco cakucereza wosowa.
29 8 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, 9 kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva.