7 Ndipo kwa yense wa ife capatsika cisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu.
8 Cifukwa cace anena,M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,Naninkha zaufulu kwa anthu.
9 Koma ici, cakuti, Anakwera, nciani nanga komakuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?
10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.
11 Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;
12 kuti akonzere oyera mtima: ku nchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu;
13 kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa cikhulupiriro, ndi wa cizindikiritso ca Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa cidzaloca Kristu.