9 Koma ici, cakuti, Anakwera, nciani nanga komakuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?
10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.
11 Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;
12 kuti akonzere oyera mtima: ku nchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu;
13 kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa cikhulupiriro, ndi wa cizindikiritso ca Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa cidzaloca Kristu.
14 Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengeka-tengeka ndi mphepo yonse ya ciphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kucenjerera kukatsata cinyengo ca kusoceretsa;
15 koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira iye amene ali mutu ndiye Kristu;