20 ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;
21 ndi kumverana wina ndi mnzace m'kuopa Kristu.
22 Akazi Inu, mverani amuna anu ainu eni, monga kumvera Ambuye.
23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.
24 Komatu monga Eklesia amvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu zonse.
25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m'malo mwace;
26 kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;