10 Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yace.
11 Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika pokana macenjerero a mdierekezi.
12 Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m'zakumwamba.
13 Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.
14 Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira m'cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo;
15 ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;
16 koposa zonse mutadzitengeranso cikopa ca cikhulupiriro, cimene mudzakhoza kuzima naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo.