6 si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima;
7 akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai;
8 podziwa kuti cinthu cokoma ciri conse yense acicita, adzambwezera comweci Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.
9 Ndipo, ambuye inu, muwacitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankhu kwa iye.
10 Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yace.
11 Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika pokana macenjerero a mdierekezi.
12 Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m'zakumwamba.