Agalatiya 2 BL92

1 Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Bamaba, ndinamtenganso Tito andiperekeze.

2 Koma ndinakwera kunkako mobvumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwa amitundu; koma m'tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga cabe.

3 Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mhelene, sanamkakamiza adulidwe;

4 ndico cifukwa ca abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nao mwa Kristu Yesu, kuti akaticititse iukapolo.

5 Koma sitidawafumukira mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti coonadi ca Uthenga Wabwino cikhalebe ndi inu.

6 Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezera ine kanthu;

7 koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe

8 (pakuti iye wakucita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anacitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);

9 ndipo pakuzindikira cisomoco cinapatsidwakwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Bamaba dzanja lamanja la ciyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;

10 pokhapo kuti tikumbukile aumphawi; ndico comwe ndinafulumira kucicita.

11 Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeyandinatsutsana naye pamaso pace, pakuti anatsutsika wolakwa.

12 Pakuti asanafike ena ocokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.

13 Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Bamabanso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.

14 Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa coonadi ca Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?

15 Ife ndife Ayuda pacibadwidwe, ndipo sitiri ocimwa a kwaamitundu;

16 koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa: nchito ya lamulo, koma mwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu, ifedi tinakhulupirira kwa Yesu Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndicikhulupiriro ca Kristu, ndipo si ndi nchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi nchito za lamulo.

17 Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Kristu, tipezedwanso tiri ocimwa tokha, kodi Kristu ali mtumikiwa ucimo cifukwa cace? Msatero ai.

18 Pakuti ngati izi zomwezi ndazigumula ndizimanganso, ndidzitsimikizira ndekha ndirt wolakwa.

19 Pakuti ine mwa lamulo ndafa ku lamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.

20 Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.

21 Sindieiyesa copanda pace cisomo ca Mulungu; pakuti ngati cilungamo ciri mwa Lamulo, Kristu adafa cabe.

Mitu

1 2 3 4 5 6