1 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Kristu anaonetsedwa pa maso panu, wopacikidwa?
2 ici cokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?
3 Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?
4 Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwacabe? ngatitu kwacabe.
5 Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nacita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi nchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa cikhulupiriro?
6 Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye cilungamo,
7 cotero zindikirani kuti iwo a cikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.
8 Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi cikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.
9 Kotero kuti iwo a cikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo,
10 Pakuti onse amene atama nchito za lamulo Iiwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa,Wotembereredwa ali yense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la cilamulo, kuzicita izi.
11 Ndipo cidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro;
12 koma cilamulo sicicokera kucikhulupiriro; koma, Wakuzicita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.
13 Kristu anatiombola ku temberero la cilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa,Wotembereredwa ali yense woo paeikidwa pamtengo;
14 kutidalitso la Abrahamu mwa Yesu Kristu, licitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa cikhulupiriro.
15 Abale, ndinena monga munthu Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesacabe, kapena kuonjezapo.
16 Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace, Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Kristu.
17 Ndipo ici ndinena; Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lacabe.
18 Pakuti ngati kulowa nyumba kucokera kulamulo, sikucokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
19 Nanga cilamulo tsono? Cinaoniezeka cifukwa ca zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo cinakonzeka ndi angelo m'dzanja la Ilkhoswe.
20 Koma nkhoswe siiri ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.
21 Pamenepo kodi cilamulo citsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti cikadapatsidwa cilamulo eakukhoza kucitira moyo, cilungamo cikadacokera ndithu kulamulo.
22 Komatu lembo Iinatsekereza zonse pansi pa ucimo, kuti lonjezano la kwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.
23 Koma cisanadze cikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira cikhulupiriro cimene cikabvumbulutsidwa bwino bwino.
24 1 Momwemo cilamulo cidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, 2 kuti tikayesedwe olungama ndi cikhulupiriro.
25 Koma popeza cadza cikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.
26 3 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa cikhulupiriro ca mwa Yesu Kristu.
27 4 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.
28 5 Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; 6 pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.
29 Koma ngati muli a Kristu, muli mbeu ya Abrahamu, 7 nyumba monga mwa Lonjezano.