1 Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse;
2 komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wace.
3 Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;
4 koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wace, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,
5 kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.
6 Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wace alowe m'mitima yathu, wopfuula Abba, Atate.
7 Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.
8 Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munacitira ukapolo iyo yosakhalamilungu m'cibadwidwe cao;
9 koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofoka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuicitira ukapolo?
10 Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka.
11 Ndiopera inu, kuti kapena odadzibvutitsa ndi inu cabe.
12 Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndiri mongainu. Simunandicitira coipa ine;
13 koma mudziwa kuti m'kufoka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba:
14 ndipo cija ca m'thupi langa cakukuyesani inu simunacipeputsa, kapena sicinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Kristu Yesu mwini.
15 Pamenepo thamo lanu liri kuti? Pakuti ndikucitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.
16 Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?
17 Acita cangu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawacitire iwowa cangu.
18 Koma nkwabwino kucita cangu m'zabwino nthawi zonse, si pokha pokha pokhala nanu pamodzi ine.
19 Tiana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Kristu aumbika mwa inu,
20 koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; cifukwa ndisinkhasinkha nanu.
21 Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva cilamulo?
22 Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana amuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.
23 Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa Ionjezano, Izo ndizo zophiphiritsa;
24 pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa ku phiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.
25 Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, m'Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ace.
26 Koma, Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.
27 Pakuti kwalembedwa,Kondwera, cumba iwe wosabala;Yimba nthungululu, nupfuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala;Pakuti ana ace a iye ali mbeta acuruka koposa ana a iye ali naye mwamuna.
28 Koma ife, abale, monga Isake, tiri ana a lonjezano.
29 Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano,
30 Koma lembo linena ciani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wace, pakuti sadzalowa nyumba mwanawa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.
31 Cifukwa cace, abale, z sitiri ana a mdzakazi, komatu a mfulu.