Agalatiya 5 BL92

Asunge ufulu wa Cikristu

1 Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; cifukwa cace cirimikani, musakodwenso ndi gori la ukapolo.

2 Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Kristu simudzapindula naye kanthu.

3 Ndicitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kucita cilamulo conse.

4 Mulibe kanthu ndi Kristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana naco cisomo.

5 Pakuti ife mwa Mzimu, kucokera m'cikhulupiriro, tilindira ciyembekezo ca cilungamo,

6 Pakuti mwa Kristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu cikhulupiriro cakucititsa mwa cikondi.

7 Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere coonadi?

8 Kukopa kumene sikucokera kwa iye anakuitanani.

9 Cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse.

10 Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza citsutso cace.

11 Koma ine, abale, ngati ndilalikiransoindulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.

12 Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.

13 Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; cokhaco musacite nao ufulu wanu cothandizira thupi, komatu mwa cikondi citiranani ukapolo.

14 Pakuti mau amodzi akwaniritsa cilamulo conse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

15 Koma ngati mulumana ndi kudyana, cenjerani mungaonongane.

Nchito za thupi ndi zipatso za Mzimu

16 Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.

17 Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.

18 Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.

19 Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano,

20 nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru,

21 kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

22 Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,

23 cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

24 Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace.

25 1 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

26 2 Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.

Mitu

1 2 3 4 5 6