Agalatiya 1 BL92

1 PAULO, mtumwi (wosacokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa iye kwa akufa),

2 ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya:

3 Cisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu,

4 amene anadzipereka yekha cifukwa ca macimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa cifuniro ca Mulungu ndi Atate wathu;

5 yemweyo akhale nao ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

Kutunsika kwa Agalatiya Utumiki wa Paulo ucokera kwa Mulungu

6 Ndizizwa kuti msanga motere mulikutunsika kwa iye amene anakuitanani m'cisomo ca Kristu, kutsata uthenga wabwino wina;

7 umene suli wina; koma pali ena akubvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Kristu.

8 Koma ngakhale ife, kapena mngelo wocokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.

9 Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani uthenga wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.

10 Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Kristu.

11 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.

12 Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa bvumbulutso la Yesu Kristu.

13 Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Ciyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,

14 ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Ciyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wacangu koposa pa miyambo ya makolo anga.

15 Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa cisomo cace,

16 kuti abvumbulutse Mwana wace mwa ine, kuti ndimlalikire iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsana ndi thupi ndi mwazi:

17 kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.

18 Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.

19 Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

20 Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.

21 Pamenepo ndinadza ku mbali za Suriya ndi Kilikiya.

22 Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Kristu;

23 koma analinkumva kokha, kuti, iye wakutilondalonda ife kale, tsopane alalikira cikhulupiriroco ada cipasula kale;

24 ndipo analemekeza Mulungu mwaine.

Mitu

1 2 3 4 5 6