2 Akorinto 13 BL92

1 Nthawi yacitatu iyi ndirinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.

2 Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kaciwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adacimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;

3 popeza mufuna citsimikizo ca Kristu wakulankhula mwa ine; amene safoka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;

4 pakuti anapacikidwa m'ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tiri ofok a mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

5 Dziyeseni nokha, ngati muli m'cikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Kristu ali mwa inu? mukapanda kukhala osatsimikizidwa.

6 Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitiri osatsimikizidwa.

7 Ndipo tipemphera Mulungu kuti musacite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke obvomerezeka, koma kuti inu mukacite cabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.

8 Pakuti sitikhoza kanthu pokana coonadi, koma pobvomereza coonadi.

9 Pakuti tikondwera, pamene ife tffoka ndi inu muli amphamvu; icinso tipempherera, ndicoungwiro wanu.

10 Cifukwa ca ici ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndiri pomwepo ndingacite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.

11 Cotsalira, abale, kondwerani, Mucitidwe angwiro; mutorithozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa cikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.

12 Lankhulanani ndi cipsompsono copatulika.

13 Oyera mtima onse alankhula inu,

14 Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mulungu, ndi ciyanjano ca Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13