2 Akorinto 6 BL92

Kudzikana kwa Paulo m'utumiki wace

1 Ndipo a ocita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire cisomo ca Mulungu kwacabe inu,

2 (pakuti anena,M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,Ndipo m'tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza;Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la cipulumutso);

3 osapatsa cokhumudwitsa konse m'cinthu ciri conse, kuti utumikiwo usanenezedwe;

4 koma m'zonse tidzitsimikfzira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,

5 m'mikwingwirima, m'ndende, m'mapokoso, m'mabvutitso, m'madikiro, m'masalo a cakudya;

6 m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;

7 m'mau a coonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa camuna ca cilungamo kulamanja ndi kulamanzere,

8 mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; mongaosoceretsa, angakhale ali oona;

9 monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani, tiri ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;

10 monga akumva cisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, lroma akulemeretsa ambiri; mensa okhala opanda-kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Awadandaulira akhale oyera mtima

11 M'kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.

12 Simupsinjika mwa ife, koma mupsiniika mumtima mwanu.

13 Ndipo kukhale cibwezero comweci (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.

14 Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti cilungamo cigawanabwanji ndi cosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji nw mdima?

15 Ndipo Kristu abvomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira?

16 Ndipo ciphatikizo cace ncanji ndi kacisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife kacisi wa, Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipe ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

17 Cifukwa cace,Turukani pakati Pao, ndipo patukani, ati Ambuye,Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka;Ndipo Ine ndidzalandira inu,

18 Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate,Ndi inu mudzakhala kwa Ine ana amunandi akazi,anena Ambuye Wamphamvuyonse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13