1 Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza ku masomphenya ndi mabvumbulutso a Ambuye.
2 Ndidziwa munthu wa mwa Kristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwacitatu.
3 Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu),
4 kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.
5 Cifukwa ca wotereyo ndidzadzitamandira; koma cifukwa ca Ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m'zofoka zanga,
6 Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena coonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.
7 Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, cifukwa ca ukulu woposa wa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelowa Satana kutianditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.
8 Za ici ndinapemphera Ambuye katatu kuti cicoke rkwafne.
9 Ndipo ananena kwa ine, Cisomo canga cikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufoko. Cifukwa cace makamaka ndidzadzitamandira rriokondweratu m'maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.
10 Cifukwa cace ndisangalala m'tnaufoko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, cifukwa ca Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wamphamvu.
11 Ndakhala wopanda nzeru, mwandtcititsa kutero; pakuti inu nunayenera kundibvomereza; pacuti sindiperewera ndi atumwiopoiatu m'kanthu konse, ndingakhale adiri cabe.
12 Zizindikilotu za ntumwi zinacitika pakati pa inu, ri'cipiriro conse, ndi zizindikilo, ndi cozizwa, ndi zamphamvu.
13 Pakuti kuli ciani cimene munacepetsedwa naco ndi Mipingo yotsala yina, agati, si ici kuti ine ndekha sindirasaukitsa inu? Ndikhululukireni oipa ici.
14 Taonani, nthawi yaitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa nu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; cakuti ana sayenera kuunjikira atate adi amai, koma atate ndi amai kumjikira ana.
15 Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse cifucwa ca miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kocuruka koposa, kodi ndikondedwa kocepa?
16 Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wocenjera ine, ndinakugwirani ndi cinyengo.
17 Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakucenjererani naye kodi? Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye.
18 Kodi Tito anakucenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?
19 Mumayesa tsopano Uno kuti tirikuwiringula kwa, inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Kristu. Koma zonse, okondedwa, ziri za kumangirira kwanu.
20 Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale cotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
21 kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandicepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri 1 a iwo amene adacimwa kale, osalapa pa codetsa, ndi cigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anacita.