1 Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi cisoni.
2 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu cisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, kama iye amene ndammvetsa cisoni?
3 Ndipo ndinalemba ici comwe, kuti pakudza ndisakhale naco cisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti cimwemwe canga ndi canu ca inu nonse.
4 Pakuti m'cisautso cambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni cisoni, koma kuti mukadziwe cikondi ca kwa inu, cimene ndiri naco koposa.
5 Koma ngati wina wacititsa cisoni, sanacititsa cisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse.
6 Kwa wotereyo cilango ici cidacitika ndi ambiri cikwanira;
7 kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo mgamizidwe ndi cisoni cocurukaco.
8 Cifukwa cace ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo cikondi canu.
9 Pakuti cifukwa ca ici ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.
10 Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti cimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndacicita cifukwa ca inu, pamasopa Kristu;
11 kuti asaticenierere Satana; pakuti sitikhala osadziwa macenjerero ace.
12 Koma pamene ndinadza ku Trowa kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Kristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,
13 ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Makedoniya.
14 Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'cigonjetso mwa Kristu, namveketsa pfungo la cidziwitso cace mwa ife pamalo ponse.
15 Pakuti ife ndife pfungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo la imfa kuimfa;
16 koma kwa ena pfungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?
17 Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akucita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa coona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.