2 Akorinto 3 BL92

1 Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otibvomerezetsa kwa inu, kapena ocokera kwa inu?

2 Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;

3 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosatim'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.

4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu:

5 si kuti tiri okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mocokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kucokera kwa Mulungu;

6 amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la cilembo, koma la mzimu; pakuti cilembo cipha, koma mzimu ucititsa moyo.

7 Komangati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolocedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sanathe kuyang'anitsa pankhope yace ya Mose, cifukwa ca ulemerero wa nkhope yace, umene unalikucotsedwa:

8 koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala m'ulemerero?

9 Pakuti ngati utumiki wa citsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa cilungamo ucurukira muulemerero kwambiri.

10 Pakutinso cimene cinacitidwa ca ulemerero sicinacitidwa ca ulemerero m'menemo, cifukwa ca ulemerero woposawo.

11 Pakuti ngati cimene cirikucotsedwa cinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri cotsalaco ciri m'ulemerero.

12 Pokhala naco tsono ciyembekezo cotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukuru,

13 ndipo si monga Mose, amene anaika cophimba pa nkhope yace, kuti ana a lsrayeli asayang'anitse pa cimariziro ca cimene cinalikucotsedwa;

14 koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa lcuwerenga kwa pangano lakale cophimba comweci cikhalabe cosabvundukuka, cimene cirikucotsedwa mwa Kristu.

15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, cophimba cigona pamtima pao.

16 Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, cophimbaco cieotsedwa.

17 Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'cithunzihunzi comweci kucokera kuulenerero kumka kuulemerero, monga ngati kucokera kwa Ambuye Mzimu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13