2 Akorinto 7 BL92

Paulo akondwerapa kudza kwa Tito, ndi pa zipatso za kalata wace woyamba

1 Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsirfza ciyero m'kuopa Mulungu.

2 Tipatseni malo; sitinamcitira munthu cosalungama, sitinaipsa munthu, sitinacenjerera munthu.

3 Sindinena ici kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.

4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga cifukwa ca inu nkwakukuru; ndidzazidwa naco citonthozo, ndisefukira naco cimwemwe m'cisautso cathu conse.

5 Pakutinso pakudza ife m'Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.

6 Koma iye amene atonthoza odzicepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwace kwa Tito;

7 koma si ndi kufika kwace kokha, komanso ndi citonthozo cimene anatonthozedwa naco mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, cangu canu ca kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa,

8 Kuti ngakhale ndakumvetsani cisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani cisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.

9 Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.

10 Pakuti cisoni ca kwa Mulungu citembenuzira mtima kueipulumutso, cosamvetsanso cisoni; koma cisonicadziko lapansi cicita imfa.

11 Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.

12 Cifukwa cace ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinacita cifukwa ca iye amene anacita coipa, kapena cifukwa ca iye amene anacitidwa coipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.

13 Cifukwa ca icitatonthozedwa; ndipo m'citonthozo cathu tinakondwera koposa ndithu pa cimwemwe ca Tito, kuti mzimu wace unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.

14 Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye cifukwa ca inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'coonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala coonadi.

15 Ndipo cikondi ceni ceni care cicurukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.

16 Ndikondwera kuti m'zonse ndilimbika mtima za inu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13