2 Akorinto 4 BL92

Paulo alalikira Yesu yekha yekha

1 Cifukwa cace popeza tiri nao utumiki umene, monga talandira cifundo, sitifoka;

2 koma takaniza zobisfka za manyazi, osayendayenda mocenjerera, kapena kucita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a coonadi tidzibvomeretsa tokha ku cikumbu mtima ca anthu onse pamaso pa Mulungu.

3 Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;

4 mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unacititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti ciwalitsiro ca Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali cithunzithunzi ca Mulungu, cisawawalire.

5 Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Kristu Yesu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, cifukwa ca Kristu.

6 Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kuturuka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa ciwalitsiro ca cidziwitso ca ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.

7 Koma tiri naco cuma ici m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosacokera kwa ife;

8 ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi;

9 olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

10 nthawi zonse tirikusenzasenza m'thupi kufa kwace kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu.

11 Pakuti ife amene tiri ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, cifukwa ca Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa.

12 Cotero imfa icita mwa ife, koma moyo mwa inu.

13 Koma pokhala nao mzimu womwewo wa cikhulupiriro, monga mwa colembedwaco, ndinakhulupira, cifukwa cace ndinalankhula; ifenso tikhulupira, cifukwa cace tilankhula;

14 podziwa kuti iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.

15 Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti cisomoco, cocurukitsidwa mwa unyinjiwo, cicurukitsire ciyamiko ku ulemerero wa Mulungu.

Cipatso ca kumva zowawa. Zosaoneka zilinganizidwa ndi zooneka

16 Cifukwa cace sitifoka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja ubvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

17 Pakuti cisautso cathu copepuka ca kanthawi citicitira ife kulemera koposa kwakukuru ndi kosatha kwa ulemerero;

18 popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka ziri za nthawi, koma zinthu zosaoneka ziri zosatha.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13