1 Ndipo tikudziwitsani, abale, cisomo ca Mulungu copatsika mwa Mipingo ya ku Makedoniya,
2 kuti m'citsimikizo cacikuru ca cisautso, kucurukitsa kwa cimwemwe cao, ndi kusauka kwaokweni kweni zidacurukira ku colemera ca kuolowa mtima kwao.
3 Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndicitapo umboni, inde koposa mphamvu yao,
4 anacita eni ace, natiumirfza ndi kutidandauliraza cisomoco, ndi za ciyanjano ca utumiki wa kwa oyera mtima;
5 ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa cifuniro ca Mulungu.
6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, comweconso atsirize kwa inu cisomo icinso.
7 Koma monga mucurukira m'zonse, m'cikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'cidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'cikondi canu ca kwa ife, curukaninso m'cisomo ici.
8 Sindinena ici monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena coonadi ca cikondi canunso.
9 Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera.
10 Ndipo m'menemo odichula coyesa ine; pakuti cimene cipindulira inu, amene munayamba kale caka capitaci si kucita kokha, komanso kufunira.
11 Koma tsopano tsirizani kucitaku; kuti monga kunali cibvomerezo ca kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwacem'cimene muli naco.
12 Pakuti ngati cibvomerezoco ciri pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali naco, si monga cimsowa.
13 Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;
14 koma mwa kulingana kucuruka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kucuruka kwao kukwanire kusowa kwanu,
15 Kuti pakhalecilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsacambiri sicinamtsalira; ndi iye wosonkhetsa pang'ono sicinamsowa.
16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.
17 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala halo khama loposa, anaturukira kunka kwil inu mwini wace.
18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwace m'Uthenga Wabwino kuli m'Mipingo yonse;
19 ndipo si ici cokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'cisomo ici, cimene ticitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa cibvomerezo cathu;
20 ndi kupewa ici kuti wina angatichule za kucurukira kumene tikutumikira;
21 pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.
22 Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizirakawiri kawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukuru kumene ali nako kwa inu,
23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wocita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Kristu.
24 Cifukwa cace muwatsimikizire iwo citsimikizo ca cikondi canu, ndi ca kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.